wokhudza
Cholinga chathu ndikulemekeza komanso kukwanilitsa lamulo lomaliza lomwe Mbuye wathu Yesu Khritsu anatisiyila "Mukani, phunzitsani anthu amitundu yonse" (Mateyu 28:19).
Timasindika ndi kukonza mapulogalamu omwe ali okhazikika pa Mau a Mulungu. Mapulogamalamuwa amakhudza ntchito zofalitsa uthenga wabwino, komanso kupanga ophunzila. Mauthenga anthu onse amaikidwa mwa nkhani ndi cholinga chofuna kufotokozela choonadi cha Malemba.
Pakadali pano timakonza mapulogalamu a mitundu isanu yosiyana. Izi zimathandiza aulutsi kumasuka pa kukonzekeza za kuulutsa masewerowa. Timalunjika kwambiri pofuna kudziwitsa anthu za chikhulupililo mwa Yesu Khritsu ngati Mbuye ndi Mpulumutsi. Timachita izi kudzera mu masewero komanso m’kukambilana Mau, zimene zimaonetsa uthenga omwe uli mu Baibulo ndi nkhani ya Yesu, mu njira yomwe anthu kulikonse atha kuwamvetsetsa. Mapulogalamuwa amagawidwa padziko lonse kudzela pa wayilesi ndi njira zina zoulutsila mau.